Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 8:24 - Buku Lopatulika

24 Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Nchifukwa chake ndakuuzani kuti mudzafera m'machimo anu. Pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine Ndilipo, mudzaferadi m'machimo anu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:24
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.


Koma wondichimwira apweteka moyo wake; onse akundida ine akonda imfa.


Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.


Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri.


Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.


Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.


Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.


Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.


Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.


Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.


Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.


Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.


Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.


Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.


Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.


Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;


tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa