Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 54 - Buku Lopatulika


Davide apempha Mulungu amlanditse
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Chilangizo cha Davide. Muja Azifi anamuka nauza Saulo, kuti, Kodi Davide sabisala kwathu nanga?

1 Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu, ndipo mundiweruze ndi mphamvu yanu.

2 Imvani pemphero langa, Mulungu; tcherani khutu mau a pakamwa panga.

3 Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.

4 Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga, Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.

5 Adzabwezera choipa adani anga, aduleni m'choonadi chanu.

6 Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu, ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.

7 Pakuti anandilanditsa m'nsautso yonse; ndipo ndapenya ndi diso langa icho ndakhumbira pa adani anga.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa