Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

118 Mau a Mulungu Pa Nkhani ya Kutopa ndi Kulefuka

Ndimadziwa kuti nthawi zina umamva kutopa. Kutopa thupi, kutopa maganizo, ngakhale kutopa mzimu. Inenso ndimadziwa bwino lomwe kutopa kumeneko.

Koma pali uthenga wabwino mu Bukhu Lopatulika, mu buku la Yesaya. Limatiuza kuti anthu amene akuyembekezera Ambuye adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati chiwombankhanga, adzathamanga osatopa, ndipo adzayenda osakomoka. Ukuganiza kuti zimenezi zingatithandize bwanji pamene tikumva kutopa?

Mu Masalimo, wamasalmo akutiuza kuti tipeze mpumulo mwa kutaya nkhawa zathu zonse pa Ambuye, podziwa kuti Iye ndiye amene amatiteteza. Sitingathe kunyamula mavuto athu tokha ayi. Ambuye ndiye mphamvu yathu.

Yesu mwini, mu Uthenga Wabwino wa Mateyu, anati: “Bwerani kwa Ine nonsenu amene mukutopa ndi kunyamula katundu wolemera, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.” Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri, eti? Tikatopa, tiyeni tipite kwa Yesu kuti tipeze mpumulo.

Choncho, musalole kuti kutopa kukugonjetse. Ambuye ali nafe nthawi zonse, ndipo adzatipatsa mphamvu zopitirira patsogolo. Zikomo kwambiri.


Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.

Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?

Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 33:14

Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 31:25

Pakuti ndakhutidwa mtima wolema, ndadzazanso mtima uliwonse wachisoni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:29-31

Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.

Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu:

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:45

Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:2

Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1-3

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.

Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 69:3

Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:1-2

Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.

Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu.

Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 17:29

ndi uchi ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng'ombe, kuti adye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m'chipululumo.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 22:45

Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi chisoni,

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 23:4

Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:26

Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 25:18

kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofooka akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaope Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 8:4

Ndipo Gideoni anafika ku Yordani, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali chilondolere.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 16:14

Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 4:6

ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 4:21

Pamenepo Yaele mkazi wa Hebere anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m'dzanja lake namdzera monyang'ama, nakhomera chichiri chilowe m'litsipa mwake; ndipo chinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 21:15

Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 6:6

Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:34

Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 32:3-4

Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse.

Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 4:8

Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 45:3

Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:27

Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 31:8

Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:19

Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 16:11

Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:28

Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:3

Pakuti talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 3:13

Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:17-18

Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa kumasautso ao onse.

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:2

Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:5-6

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:2

Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;

umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3-4

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:58

Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 4:16-18

Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;

popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:1-2

Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?

Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:28

Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 19:4-8

Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.

Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.

Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi.

Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakukanika.

Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:7

Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:15

Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:10

Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 4:10

Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:13-14

Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani!

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:1-2

Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.

palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.

Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse.

Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala.

Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.

Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.

Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.

Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:5-6

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.

Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:1

Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 1:9

Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:3-4

Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu.

Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 24:10

Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 32:17-18

Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.

Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:6-7

M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,

kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 1:3-4

Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,

wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 16:33

Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 8:10

Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 28:7

Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:3-5

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;

ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 35:3-4

Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.

Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:18-19

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:10

Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 7:6

Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:16

akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:3

Tsiku loitana ine, munandiyankha, munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 61:2

Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 51:12

Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 33:27

Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 4:17

Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 50:15

Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 4:4

Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 33:2

Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, chipulumutso chathunso m'nthawi ya mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 3:3-5

Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.

Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga, ndipo andiyankha m'phiri lake loyera.

Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo; ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:3

Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 3:16-17

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,

kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:14

Yehova agwiriziza onse akugwa, naongoletsa onse owerama.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 57:15

Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:11

ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 3:22-23

Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,

chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:10

Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 18:1

Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:1-2

Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.

Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu.

Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.

Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.

Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova.

Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.

Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede.

Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova.

Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.

Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 6:10

pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 3:13-14

Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,

ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 116:7

Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; pakuti Yehova anakuchitira chokoma.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:37

Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 2:16-17

Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,

asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mau onse abwino.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:4

Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:24

Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 16:13

Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:50

Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mau anu anandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 15:2

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:2

Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 13:4

pakuti anapachikidwa mu ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:7

Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:5

Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:5

ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:1-5

Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.

Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.

Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.

Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.

Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.

Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.

Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo.

Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso.

Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.

Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.

Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:

Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.

Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.

Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.

Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse;

amene aombola moyo wako ungaonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma:

Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Mzimu Woyera, kukhala pafupi nanu n'kokongola kwambiri, chikondi chanu chopanda malire chikundikuta ndipo mukundidzaza ndi chisomo ndi chiyanjo chanu. Ndimakulambirani chifukwa ndinu Mpulumutsi wanga, ndine cholengedwa cha manja anu, mwandilimbitsa, lero ndikubwera kwa inu ndi kudzipereka pamapazi anu chifukwa ndinu malo anga opumulira, m'mavuko anga mumandipatsa njira yotulukira, ndipo m'nkhondo yanga mumandipatsa mtendere, zikomo chifukwa chokhala nane nthawi zonse, zikomo chifukwa chondisonyeza kukhulupirika kwanu ndi chifundo chanu m'mawa uliwonse, lero ndikupemphani kuti mundipatse mphamvu zambiri, limbitsani mafupa anga ndipo musalole kuti mawondo anga afooke, ndikufuna kuchita chifuniro chanu nthawi zonse, choncho ndikuchotsa kutopa konse m'thupi langa, kutopa konse ndipo ndimatenga goli la Khristu, chifukwa mawu anu amati ndi lopepuka, tsopano ndikusiya zolemetsa zonse ndipo ndikupumula m'mawu anu, mumandikhazika mtima pansi ngati chiwombankhanga ndipo mumandipatsa mphamvu ngati za njati. Zikomo Ambuye wanga, chifukwa nthawi zonse mtima wanga umakhulupirira inu. M'dzina la Yesu, Ameni.