Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:3 - Buku Lopatulika

3 Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndafooka ndi kulira kwanga, kum'mero kwanga kwauma. M'maso mwada pamene ndikuyembekezera Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndafowoka ndikupempha chithandizo; kummero kwanga kwawuma gwaa, mʼmaso mwanga mwada kuyembekezera Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:3
18 Mawu Ofanana  

Koma maso a oipa adzagoma, ndi pothawirapo padzawasowa, ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.


Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi, ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa;


Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu, ndi mau a chilungamo chanu.


Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu, ndikuti, Mudzanditonthoza liti?


Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete.


Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge, pakuti ndayembekezera Inu.


Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani? Chiyembekezo changa chili pa Inu.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.


Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.


Mkwiyo wanu utsamira pa ine, ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.


Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.


Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa