Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:4 - Buku Lopatulika

4 Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Anthu odana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kupambana tsitsi la kumutu kwanga. Ndi amphamvu anthu ongofuna kundiwononga, ndi kundineneza ndi mabodza ao. Kodi ndiyenera kubweza zimene sindinabe?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwo amene amadana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga; ambiri ndi adani anga popanda chifukwa, iwo amene akufunafuna kundiwononga. Ndikukakamizidwa kubwezera zomwe sindinabe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:4
14 Mawu Ofanana  

Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.


Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.


Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova,


Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni; lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.


Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa