Masalimo 6 - Buku LopatulikaDavide apempha chifundo kwa Mulungu Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto, pa Seminiti. Salimo la Davide. 1 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, ndipo musandilange muukali wanu. 2 Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga. 3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu; ndipo Inu, Yehova, kufikira liti? 4 Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu. 5 Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu; m'mandamo adzakuyamikani ndani? 6 Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga. 7 Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni; lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa. 8 Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga. 9 Wamva Yehova kupemba kwanga; Yehova adzalandira pemphero langa. 10 Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu adani anga onse; adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi