Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 6:3 - Buku Lopatulika

3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu; ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu; ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mtima wanganso wazunzika kwambiri. Nanga Inu Chauta, zimenezi zidzakhala zikuchitika mpaka liti?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 6:3
15 Mawu Ofanana  

Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa, ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.


Kodi Ambuye adzataya nthawi yonse? Osabwerezanso kukondwera nafe.


Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.


Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka?


Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.


Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.


Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa