Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 6:2 - Buku Lopatulika

2 Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndichitireni chifundo, Inu Chauta, chifukwa chakuti ndine wofooka. Limbitseni, Inu Chauta, chifukwa m'nkhongono mwanga mwaweyeseka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 6:2
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana.


Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.


Pakuti apweteka, namanganso mabala; alasa, ndi manja ake omwe apoletsa.


Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.


Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.


Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse.


Pakuti mivi yanu yandilowa, ndi dzanja lanu landigwera.


Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu; ndipo m'mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa.


Pakuti m'chuuno mwanga mutentha kwambiri; palibe pamoyo m'mnofu mwanga.


Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera, kuti mafupawo munawathyola akondwere.


ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.


Yehova, mundilangize, koma ndi chiweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.


Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.


Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.


Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mchiritsenitu, Mulungu.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa