Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -

Masalimo 6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero


Salimo 6
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.

1 Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu.

2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.

3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?

4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda?

6 Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.

7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga.

8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga.

9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa.

10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

The Word of God in Contemporary Chichewa

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®

Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®

Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Biblica, Inc.
Titsatireni:



Zotsatsa