Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 6:10 - Buku Lopatulika

10 Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu adani anga onse; adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu adani anga onse; adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Adani anga onse adzagonjetsedwa mwa manyazi ndipo adzagwidwa ndi mantha, modzidzimuka onse adzathaŵa motaya mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 6:10
23 Mawu Ofanana  

Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu; inde, bwereraninso mlandu wanga ngwolungama.


Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.


Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.


Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake, nadzawaopsa mu ukali wake.


Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi; adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa.


Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.


Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu.


Anatulutsa manja ake awagwire iwo akuyanjana naye, anaipsa pangano lake.


Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.


Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.


Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.


Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.


Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.


Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa