Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 7:1 - Buku Lopatulika

1 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu; mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu; mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta, Mulungu wanga, ndikuthaŵira kwa Inu. Mundilanditse kwa onse ondithamangitsa. Mundipulumutse,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu; pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 7:1
29 Mawu Ofanana  

Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?


Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;


Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.


Pakuti Inu muyatsa nyali yanga; Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.


Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, ndisachite manyazi; adani anga asandiseke ine.


Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.


Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.


kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.


Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.


Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.


Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.


Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.


Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m'chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa.


Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.


Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.


Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,


Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoti.


Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.


Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa