Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 6:6 - Buku Lopatulika

6 Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndatopa nkubuula kwambiri. Ndimanyowetsa bedi langa ndi misozi usiku uliwonse. Ndimakhathamiza pogona panga chifukwa cha kulira kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 6:6
23 Mawu Ofanana  

Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.


Mabwenzi anga andinyoza; koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu.


Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa; kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwake.


momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pake. Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.


Akufa salemekeza Yehova, kapena aliyense wakutsikira kuli chete:


Mverani, Yehova, ndipo ndichitireni chifundo, Yehova, mundithandize ndi Inu.


Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu; ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu.


Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.


Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.


Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi, chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?


Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.


Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa