Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 6:8 - Buku Lopatulika

8 Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chokani apa, inu nonse ochita zoipa, Chauta wamva kulira kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 6:8
16 Mawu Ofanana  

M'diso mwanga muchita chizirezire chifukwa cha chisoni, ndi ziwalo zanga zonse zilibe chithunzi.


Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa, maso anga kumisozi, mapazi anga, ndingagwe.


Mundichokere ochita zoipa inu; kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.


Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine.


Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.


Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga, ndipo andiyankha m'phiri lake loyera.


Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.


Muwerenga kuthawathawa kwanga, sungani misozi yanga m'nsupa yanu; kodi siikhala m'buku mwanu?


Pakuti anthu adzakhala mu Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kufuula kwako; pakumva Iye adzayankha.


Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.


Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.


munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.


ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa