ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.
Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.
Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha. Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu. Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ochita zozizwa? Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera. Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau? Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu.
Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau?
Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere. Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau padziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau. Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine. Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo. Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule. Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu. Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso. Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena? Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe. Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse; koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime. Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi. Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu. Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye. Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira. Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka? Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse; zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu. Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira. Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu. Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire. Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa. Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo. Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe; ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri; pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima. Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena. Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo. Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha? Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye. Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa. Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime. Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo. Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka. Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.
Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.
Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere. Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau padziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau. Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine. Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo. Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule. Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu. Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso. Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena? Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe. Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse; koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime. Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.
Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.
Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule. Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.
Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.
Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.
Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.
Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena? Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe.
Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse; koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.
Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;
Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.
Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine.
Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka? Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse; zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.
Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira. Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.
Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire. Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa. Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo. Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe; ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri; pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.
Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime. Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo. Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa. Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota. Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero. Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi. Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera. Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe. Koma anali mu Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo. Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'chilankhulidwe chake cha iye yekha.
ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu.
Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,
Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.
Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro; kapena yakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako; kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe. Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu. Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu. Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.
Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo. Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu, ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani. Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho. Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto. Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu. Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao; Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi;
Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.
Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;
Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Musazime Mzimuyo; Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Musanyoze manenero; Yesani zonse; sungani chokomacho,
pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa; amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuniro cha Mulungu.
Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau padziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.
Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane; amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera: pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.
Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife; ndipo sanalekanitse ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'chikhulupiriro.