Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:130 - Buku Lopatulika

130 Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

130 Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

130 Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

130 Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika; ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:130
17 Mawu Ofanana  

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.


Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.


Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.


Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.


kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;


Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa