Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 14:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nʼkanakonda kuti aliyense mwa inu atamayankhula malilime, koma ndi bwino kuti muzinenera. Amene amanenera amaposa amene amayankhula malilime, pokhapokha atatanthauzira kuti mpingo upindule.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 14:5
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.


Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;


Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.


ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.


Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.


Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,


Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere.


Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa