1 Akorinto 14:6 - Buku Lopatulika6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m'vumbulutso, kapena m'chidziwitso, kapena m'chinenero, kapena m'chiphunzitso? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m'vumbulutso, kapena m'chidziwitso, kapena m'chinenero, kapena m'chiphunzitso? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Abale, mudzapindulanji ngati ndibwera kwa inu nkumadzalankhula m'zilankhulo zosadziŵika? Simudzapindula konse ndi kulankhula kwangako, ngati m'mau angawo mulibe zina zimene Mulungu wandiwululira, kapena zina zopatsa nzeru, kapena zina zimene Mulungu andipatsa kuti ndinene, kapenanso phunziro lina. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Tsono, abale, mudzapindula chiyani nditabwera kwa inu ndi kukuyankhulani mʼmalilime? Koma mudzapindula ngati nditakubweretserani vumbulutso lina lake, kapena chidziwitso, kapena chiphunzitso. Onani mutuwo |