Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 45:3 - Buku Lopatulika

3 Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Iwe Baruki udati, ‘Tsoka kwa ine, poti Chauta wandiwonjezera chisoni pa mavuto anga onse. Ndatopa nako kubuula kwanga, sindikutha kupeza mpumulo konse!’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iwe unati, ‘Kalanga ine! Yehova wawonjezera chisoni pa mavuto anga. Ine ndatopa ndi kubuwula ndipo sindikupeza mpumulo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 45:3
28 Mawu Ofanana  

Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa; kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwake.


Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!


Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani!


Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.


Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.


Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni; lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.


Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.


Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.


Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki:


Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.


Zoipa zao zonse zidze pamaso panu, muwachitire monga mwandichitira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse, pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga.


Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake.


Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka;


Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.


Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.


Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa