Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 45:4 - Buku Lopatulika

4 Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chauta adandiwuza kuti ndilankhule mau aŵa kwa iwe Baruki, ‘Chimene ndidamanga, ndikuchigwetsa. Chimene ndidabzala, ndikuchizula. Umu ndi m'mene ndidzachitire ndi dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma Yehova akukuwuza kuti, “Ndidzagwetsa chimene ndinamanga ndipo ndidzazula chimene ndinadzala. Ndidzachita zimenezi mʼdziko lonse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 45:4
12 Mawu Ofanana  

mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;


penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse, umange, ubzale.


Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.


Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.


Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.


Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata mu Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.


Chifukwa chake taonani, ndidzamkopa ndi kunka naye kuchipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima.


Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa