Mayeso ndi nthawi imene timakopeka kuchita zinthu zosakondweretsa Mulungu (zoyipa) ndi lonjezo loti tidzapeza chisangalalo kapena phindu. Tonsefe, zaka zathu zilibe kanthu, tidzayesedwa pa moyo wathu wonse, koma ndi bwino kukumbukira kuti mayeso si uchimo. Mayeso ndi mwayi wochita zinthu zosakondweretsa Mulungu, kutanthauza kudzikondweretsa tokha, kapena kusankha kusadzikondweretsa tokha ndi kukondweretsa Mulungu ponena AYI ku mayeso.
Zinthu zambiri padziko lapansi, ngakhale anthu, zidzagwiritsidwa ntchito kutikopa kuchimwa, kuti titsatire Satana m'malo motsatira Mulungu. Gawo la moyo uno ndikuphunzira kugonjetsa mayeso ndi kusankha chabwino pa choipa. Kuyambira kugwa kwa Adamu ndi Eva, anthu akhala akulolera zilakolako za dziko lapansi ndi kugonjera zilako lako za thupi. Monga ana a Mulungu, tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha kuti tigonjetse mayeso ndi kusankha kutsatira Yesu Khristu mwa kufuna kwathu.
Munthu wothawa mayeso si wamantha, ndi wolimba mtima pamaso pa Mulungu! (Yakobo 1:12)
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu:
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye. Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye. Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.
Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira. Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.
Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.
Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.
Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.
Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.
Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.
Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
Mtima wako usapatukire kunjira ya mkaziyo, usasochere m'mayendedwe ake. Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; ndipo ophedwa ndi iye achulukadi. Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda, yotsikira kuzipinda za imfa.
Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko.
Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.
Pakuti pakuyendayenda m'thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi, (pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga); ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake.
Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa. Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire.
koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.
Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye. Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m'moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri. Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa mu Gehena wamoto, uli ndi maso awiri.
Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena. Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.
Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake?
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m'kamwa mwake muti see koposa mafuta. Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo, ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse. Mayendedwe ake atsikira kuimfa; mapazi ake aumirira kumanda;
Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu:
Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu. Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,
Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.
Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.