Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 2:18 - Buku Lopatulika

18 Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 2:18
16 Mawu Ofanana  

Koma inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m'mayesero anga;


Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.


Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m'dzanja la Atate.


Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.


Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.


akhale wokhoza kumva chifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi chifooko;


Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;


Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera,


Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa