Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 2:17 - Buku Lopatulika

17 Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 2:17
37 Mawu Ofanana  

ndi ansembewo anawapha, nachita nsembe yauchimo ndi mwazi wao paguwa la nsembe, kuchita chotetezera Aisraele onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yauchimo zikhale za Aisraele onse.


Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.


ndi mwanawankhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wochokera kumadimba a Israele, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwachitira chotetezera, ati Ambuye Yehova.


Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.


Tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo uchitire momwemo aliyense wolakwa ndi wopusa; motero muchitire Kachisiyo chomtetezera.


Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.


natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.


nachitire chotetezera malo opatulika, chifukwa cha kudetsedwa kwa ana a Israele, ndi chifukwa cha zolakwa zao, monga mwa zochimwa zao zonse; nachitire chihema chokomanako momwemo, chakukhala nao pakati pa zodetsa zao.


Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.


Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde paguwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.


Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala.


Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.


Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.


ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;


Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'chifuwa chanu m'ntchito zoipazo,


ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;


Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.


Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;


Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu.


Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;


amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yake yonse.


Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi;


Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo:


wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


akhale wokhoza kumva chifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi chifooko;


Koteronso Khristu sanadzilemekeze yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye, Mwana wanga ndi Iwe, lero Ine ndakubala Iwe.


m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Pakuti chilamulo chimaika akulu a ansembe anthu, okhala nacho chifooko; koma mau a lumbirolo, amene anafika chitapita chilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda chilema kunthawi zonse.


Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu mu Kumwamba,


Pakuti mkulu wa ansembe aliyense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka.


Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa