Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 4:15 - Buku Lopatulika

15 Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 4:15
20 Mawu Ofanana  

Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.


Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.


Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.


Koma inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m'mayesero anga;


kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.


Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji?


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.


akhale wokhoza kumva chifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi chifooko;


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.


amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;


Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa