Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:45 - Buku Lopatulika

45 Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Pambuyo pake adabwera kwa ophunzira ake nati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Ndipotu nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa anthu ochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo, “Kodi mukanagonabe ndi kupumula? Taonani, ora layandikira ndipo Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa ochimwa.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:45
14 Mawu Ofanana  

Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.


Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.


Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wina wake, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.


Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda.


Ndipo anawasiyanso, napemphera kachitatu, nateronso mau omwewo.


Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.


Ndipo Iye anapita m'tsogolo pang'ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire.


Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.


Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe.


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa