Ndikudziwa kuti nthawi zina mtima wako umadzadza ndi kukayika. Zimachitikira aliyense, ngakhale ine. Koma pali chinthu chabwino chomwe Baibulo limatiphunzitsa pankhani ya kukayika.
Baibulo limatiuza kuti kukayika kungatithandize kukula m'chikhulupiriro. Kutipatsa mpata wofunafuna Mzimu Woyera mozama ndikukhulupirira malonjezo a Mulungu. Chikhulupiriro chenicheni sichidalira zinthu zomwe tingaone ndi maso athu, koma chidalira zimene Mulungu watikonzera.
Tangoganizira za Davide m'Baibulo. Iye sankaopa kuuza Mulungu zakukayika kwake ndi mavuto ake. Zimenezi zimatiphunzitsa kuti kukayika sikuti ndi chinthu choipa kwambiri. Tikapereka nkhawa zathu kwa Mulungu m'pemphero ndikuwerenga Mawu ake, kukayika kumeneko kungatipatse mphamvu.
Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.
Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?
Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?
Ndipo anthu anati kwa Samuele, Ndani iye amene anati, Kodi Saulo adzatiweruza ife? Tengani anthuwo kuti tiwaphe.
Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikire, zondidabwitsa, zosazidziwa ine.
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.
Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.
Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu aliyense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupirira kuti chimene achinena chichitidwa, adzakhala nacho.
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji ovutika? Ndipo matsutsano amauka bwanji m'mtima mwanu?
Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.
Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.
Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?
Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;
ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sangathe kudzikana yekha.
Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeke chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.
Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu. Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.
Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani! Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala? Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.
Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro. Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso. Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi. Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.
Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!
Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.
Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.
Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.
amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu.
Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.
Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.
koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!
chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;
amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu; kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.
amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;
Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo chinawerengedwa kwa iye chilungamo.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.