Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati mukhala ndi chikhulupiriro, osakayika, mudzachita zimene ndauchita mkuyuzi. Koma si pokhapo ai, ngakhale mutauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ zidzachitikadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:21
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.


Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.


Ndipo ophunzira poona ichi anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga?


koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa