Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 11:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Odala ndi munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 11:6
26 Mawu Ofanana  

Odala angwiro m'mayendedwe ao, akuyenda m'chilamulo cha Yehova.


ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.


Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye.


Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.


Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.


Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena.


Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.


Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;


Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.


Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe.


Pa ichi ambiri a ophunzira ake anabwerera m'mbuyo, ndipo sanayendeyendenso ndi Iye.


Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.


Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha.


Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa