Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 10:24 - Buku Lopatulika

24 Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Anthu adamzinga namufunsa kuti, “Kodi udzaleka liti kutikayikitsa? Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, tiwuze momveka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 10:24
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.


nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?


Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula.


Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m'mitima yao za Yohane, ngati kapena iye ali Khristu;


Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?


Ayuda anatolanso miyala kuti amponye Iye.


Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.


Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.


Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?


Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.


Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa