Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


60 Mau a m'Baibulo Okhudza Moyo Wosatha

60 Mau a m'Baibulo Okhudza Moyo Wosatha

Moyo wako udzakhalapo kwamuyaya. Ukhoza kukhala ndi Mulungu kumwamba, ngati walandira Yesu Khristu ngati Mpulumutsi wako ndipo waulula machimo ako. Kapena, ukhoza kukhala ku gehena ngati ukana mphatso ya chipulumutso cha Mulungu.

Malemba Opatulika amatiuza momveka bwino kuti aliyense, opuluka ndi osapulumuka, adzakhala kwamuyaya, kumwamba kapena ku gehena. Moyo sutha pamene thupi lathu lapadziko lapansi lifa.

Mulungu watilonjeza kuti miyoyo yathu sidzangotha, komanso matupi athu adzaukitsidwa. Monga momwe Malemba amanenera, "Ambiri a iwo akugona m'fumbi lapansi adzadzuka, ena ku moyo wosatha, ndi ena ku manyazi ndi kunyozedwa kosatha." (Danieli 12:2)




Luka 20:36

Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25-26

Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:4

Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:51

Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:4

Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:54

Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:7

kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:53

Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:8

Pakuti tingakhale tili ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; chifukwa chake tingakhale tili ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:28

Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:52

ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:7

Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:19-31

Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao. ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:7

fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 49:15

Koma Mulungu adzaombola moyo wanga kumphamvu ya manda. Pakuti adzandilandira ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:16

Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:24-25

Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa; koma Mau a Ambuye akhala chikhalire. Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:28-29

Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:24-26

Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero. Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu. Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:11

ndipo utsi wa kuzunza kwao ukwera kunthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chilombocho ndi fano lake, ndi iye aliyense akalandira lemba la dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:28

M'khwalala la chilungamo muli moyo; m'njira ya mayendedwe ake mulibe imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:19

Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 12:2-3

Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha. Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:10

Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:26

Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:27

Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:46

Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:13-14

Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:22-23

Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 23:43

Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine mu Paradaiso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:16

Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24

Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 14:14

Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2-4

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai. Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho. Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima. Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye; chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo. Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama anachitacho; ndipo palibe tsankho. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:40

Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:51-54

Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa. Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:2-3

M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndili Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye. Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi? Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo. Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine. Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu. Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha. Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine. Ndipo tsopano ndakuuzani chisanachitike, kuti pamene chitachitika mukakhulupirire. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:3

Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:6

Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:42-44

Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'chivundi, liukitsidwa m'chisavundi; lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m'chifooko, liukitsidwa mumphamvu; lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:53-54

Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa. Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:16-18

Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:1

Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:8

koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m'thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:21-23

Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula. Koma ngati kukhala ndi moyo m'thupi ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha. Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:20-21

Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu; amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:13-17

Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu. Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:10

koma chaonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:27-28

Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro; kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:3-4

Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu; kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:23

inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:25

Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:11-13

Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo. Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:18

ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:7

Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:12-15

Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao. Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto. Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:4

ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:5

Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu Wamphamvuzonse, ulemerero ndi ulemu zikhale zako! Zikomo chifukwa miyoyo yonse ndi yanu, ndipo munaiilenga ikhale yamuyaya, yosatha, ndi chidziwitso cha chabwino ndi choipa. Choncho, moyo uliwonse, ngakhale pambuyo pa imfa, udzakuwerengera mlandu, ena kuti apulumuke, ena kuti akaweruzidwe kosatha, aliyense malinga ndi ntchito zake. Koma zoonadi, moyo wochimwa udzamwalira ndipo udzaukitsidwa kuti ukawoneke mavuto ndi kuzunzika kosatha. Inu munati m'mawu anu: "Pakuti idzafika nthawi imene onse ali m'manda adzamva mawu ake; ndipo iwo amene anachita zabwino adzatuluka kuuka kwa moyo; koma iwo amene anachita zoipa adzatuluka kuuka kwa chiweruzo." Ambuye wanga Yesu, zikomo chifukwa ndinu wolungama ndipo mudzaukitsa miyoyo yosavunda ya atumiki anu oyera, kuti akasangalale ndi moyo wosatha pamodzi nanu. Monga mwanenera m'mawu anu: "Moyo wosatha kwa iwo amene, popirira kuchita zabwino, amafunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chosatha." Atate, ndikupemphani kuti mpingo wanu upirire, osasunthika m’chikhulupiriro, koma tsiku lililonse tiziganizira za chipulumutso chathu ndi mantha ndi kunjenjemera. Pitirizani kuwonjezera iwo amene adzapulumutsidwa, kuti miyoyo ina nayonso iukitsidwe ku chipulumutso. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa