Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 20:36 - Buku Lopatulika

36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Iwo adzakhala ngati angelo, mwakuti sangafenso ai. Iwo ndi ana a Mulungu popeza kuti Iye adaŵaukitsa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani




Luka 20:36
20 Mawu Ofanana  

Iye wameza imfa kunthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa padziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.


Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.


Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.


Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.


Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a Kumwamba. Koma za akufa, kuti akaukitsidwa;


Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;


Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.


Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'chivundi, liukitsidwa m'chisavundi;


Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo.


amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.


Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.


ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.


Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa