Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


160 Mauthenga a Mulungu Okhudza Kusakhwima Mwauzimu

160 Mauthenga a Mulungu Okhudza Kusakhwima Mwauzimu

Ufulu wanga wauzimu unayamba pamene ndinalandira Khristu ngati Mpulumutsi wanga. Koma imeneyo ndiye kungoyamba chabe. Ulendowu uyenera kupitirira ndi kukula mwa makhalidwe ofanana ndi a Khristu. Njira imeneyi si onse okhulupirira amatsatira njira yachibadwa yokhwima. Ambiri amakhalabe Akristu osakhwima kapena a m'thupi, zomwe zimakhudza khalidwe lawo, kuwonetsa machimo ambiri ndi kusowa nzeru m'machitidwe awo.

Kukhwima kwauzimu sikubwera tsiku limodzi. Kumafunika chikhulupiriro ndi chipiriro. Munthu akhoza kukhala ndi zaka zambiri akuzindikira Khristu, koma osakulitsa ubale wake naye. Koma sizikuyenera kukhala choncho.

Aheberi 5:11-14 imati: “Pakuti pokhala ndi nthawi yayitali, muyenera kukhala aphunzitsi, koma mufunikira wina kuti akuphunzitseni kuyambira pachiyambi mfundo zoyamba za mawu a Mulungu; ndipo mwakhala ofooka, ofunika mkaka, osati chakudya chotafuna. Pakuti yense wakudya mkaka sadziwa mawu a chilungamo; pakuti ndi khanda. Koma chakudya chotafuna ndi cha anthu akuluakulu, amene pogwiritsira ntchito, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”

Ndikofunika kuunika ubale wathu ndi Mulungu ndikukonza zolakwa zathu kuti tipitirire patsogolo. Sitingathe kukhala ndi makhalidwe ndi zochita zomwezo za zaka zapitazo. Tiyenera kuyenda mokwanira ndi Yesu, kumuyika Iye pakati pa miyoyo yathu. Pokhapokha tingayende molimba mtima ndipo palibe chomwe chingatichitikire chomwe chingatisokoneze pa cholinga chathu chamuyaya mwa Mulungu.




Miyambo 9:6

Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo; nimuyende m'njira ya nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:1

Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:20

Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:1-3

Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo. Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu, ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani. Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho. Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto. Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu. Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao; Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi; ndiponso Ambuye azindikira zolingirira za anzeru, kuti zili zopanda pake. Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu; ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu; koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu. pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:3

pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:2

Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:2

lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14

Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:12-14

Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mau a chilungamo; pakuti ali khanda. Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:12

Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:22

Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 10:2

Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:6

Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:14

okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:26-27

Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:1-3

Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse; Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka. Ndiopera inu, kuti kapena ndadzivutitsa ndi inu chabe. Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndili monga inu. Simunandichitire choipa ine; koma mudziwa kuti m'kufooka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba: ndipo chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputse, kapena sichinakunyansireni, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Khristu Yesu mwini. Pamenepo thamo lanu lili kuti? Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine. Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona? Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu. Koma nkwabwino kuchita changu m'zabwino nthawi zonse, si pokhapokha pokhala nanu pamodzi ine. Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu, komatu ali wakumvera omsungira ndi adindo, kufikira nthawi yoikika kale ndi atate wake. koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; chifukwa ndisinkhasinkha nanu. Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo? Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana aamuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu. Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa; pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara. Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, mu Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake. Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu. Pakuti kwalembedwa, Kondwera, chumba iwe wosabala; imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna. Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano. Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano. Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:3

nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28

amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:18

Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:11

Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15

koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22

Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:15

Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:1

Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:6-7

Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye, ozika mizu ndi omangiririka mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24-27

Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:1-3

Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu, pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe. Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima. Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha, nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo. Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza. Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu; chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba; a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha. m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki. Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7-8

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:13-14

Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate. Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:15-17

Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:21

Yesani zonse; sungani chokomacho,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1

Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:32

Wokana mwambo apeputsa moyo wake; koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:20-21

Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera; ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11-12

Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:10

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:7

Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:5-6

Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:5-8

Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi. Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:14

ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10-11

Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:27

Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:15

Mtima wa wozindikira umaphunzira; khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:14

Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:39

Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:28

Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:29

Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:1-2

Chifukwa chake tidzatani? Tidzakhalabe mu uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke? Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi; ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu. Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu. Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo. Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo. Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai. Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo? Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho; ndipo pamene munamasulidwa kuuchimo, munakhala akapolo a chilungamo. Ndilankhula manenedwe a anthu, chifukwa cha kufooka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusaweruzika kuti zichite kusaweruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso. Msatero ai. Ife amene tili akufa ku uchimo, tidzakhala bwanji chikhalire m'menemo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1-3

Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse, inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo. Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo; ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira. Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa; monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu. Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu. Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali. Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera. lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso; Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu. Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake; amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo; amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama; amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo. Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu. ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:21

chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:11-12

Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otivuta powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu. Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:5

koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:10

ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:1-2

Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa. Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa? Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma. Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa. Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi. Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda. Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse. Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso. Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere. Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:23-24

koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:17

Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:13-14

Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:12

Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:16

Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:15

Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:45

Ndipo ndidzayenda mwaufulu; popeza ndinafuna malangizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:16-17

Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22-25

Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:4

Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:20

Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:18

Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:4-6

Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera, nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza, koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:20-21

Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama; chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro. Chisomo chikhale nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:1-3

Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa? Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi. Ndipo chidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro; koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi. Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo. Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro. Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo. Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu. Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe. Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano. Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m'dzanja la nkhoswe. Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro? Koma nkhoswe siili ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi. Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo. Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo. Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikavumbulutsidwa bwinobwino. Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro. Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi. Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu. Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu. Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano. Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:13

pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:67

Ndisanazunzidwe ndinasokera; koma tsopano ndisamalira mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:4

Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14-15

Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:13

ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:22

ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:20-21

Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo. Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:37

Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:1

Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:2-4

Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi. pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:48

Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:54

Malemba anu anakhala nyimbo zanga m'nyumba ya ulendo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:13-14

Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu. Chosungitsa chokomacho udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-13

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:14

Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:3-5

Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo: iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa; makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8-9

Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao; koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:16

Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:25

Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11-12

Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo; ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:5-6

ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye; pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:28

Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:18-19

Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu; chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:14

Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:16

Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:41

Ndipo chifundo chanu chindidzere, Yehova, ndi chipulumutso chanu, monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:14-16

monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:22

koma tsopano anakuyanjanitsani m'thupi lake mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda chilema ndi osatsutsika pamaso pake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:5

Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m'chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:14

Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:16

Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:5

Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11-12

musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:2-3

Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro? Koma nkhoswe siili ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi. Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo. Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo. Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikavumbulutsidwa bwinobwino. Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro. Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi. Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu. Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu. Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano. Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:11

Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:1

Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:2

lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-17

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:3-6

Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi; koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye; iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:8

Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:6-7

Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m'chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina; umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:130

Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:16

Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:32-33

Chifukwa chake yense amene adzavomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba. Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:27

Mundizindikiritse njira ya malangizo anu; kuti ndilingalire zodabwitsa zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23

chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:1-4

Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai. Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu. Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu. Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa. Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa. Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera. Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire. Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu. Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake. Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofooka angodya zitsamba. Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse zili zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa. Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako. Chikhulupiriro chimene uli nacho, ukhale nacho kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu. Wodala ndiye amene sadziweruza mwini yekha m'zinthu zomwe iye wazivomereza. Koma iye amene akayikakayika pakudya, atsutsika, chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chilichonse chosatuluka m'chikhulupiriro, ndicho uchimo. Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira. Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:22

Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:16

Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wachikondi, ndikufuna kukutamandani ndi kudalitsa dzina lanu loyera. Ndikubwera pamaso panu kukuthokozani chifukwa cha zonse, chifukwa ndinu wabwino ndipo chifundo chanu chimakhalapo nthawi zonse. Zikomo chifukwa cha moyo, chifukwa cha thanzi langa, chifukwa dzanja lanu lamphamvu landilimbitsa. Zikomo chifukwa cha kuleza mtima kwanu pa ine, ndipo tsiku lililonse mumandisonyeza chikondi chanu ngakhale sindiyenera. Ambuye, panopa ndikudzipereka pamaso panu, ndikuvomereza zofooka zanga. Ndikudziwa kuti ndili ndi zolakwa zambiri ndipo ndikufunika thandizo lanu kuti ndikule m'mbali zonse za moyo wanga. Ndikukupemphani kuti mudzitamandidwe mwa ine, ndipo kuti ndikhale chitsanzo chabwino kwa onse amene ali pafupi nane pankhani ya chikhulupiriro changa mwa Khristu. Ndikufuna kuyenda molimba mtima popanda manyazi, ndipo khalidwe langa likuwonetseni inu m'zonse zimene ndimachita ndi kunena. Ndikupatsani ulemerero wonse, ulemu ndi kutamandidwa kosatha, m'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa