Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Petro 2:2 - Buku Lopatulika

2 lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,

Onani mutuwo Koperani




1 Petro 2:2
21 Mawu Ofanana  

Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa?


Koma wolungama asungitsa njira yake, ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.


Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.


Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni.


Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebanoni.


Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.


Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.


Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.


Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.


Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.


mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye;


koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;


Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;


inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.


Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa