Ahebri 5:12 - Buku Lopatulika12 Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba! Onani mutuwo |