Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:25 - Buku Lopatulika

25 Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Ndangoti thapsa m'fumbi. Bwezereni moyo monga momwe mudalonjezera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Moyo wanga wakangamira fumbi; tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:25
22 Mawu Ofanana  

Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.


Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu; mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.


Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.


Penyani kuti ndikonda malangizo anu; mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu.


Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.


Taonani, ndinalira malangizo anu; mundipatse moyo mwa chilungamo chanu.


Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu; ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.


Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse; popeza munandipatsa nao moyo.


Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso.


Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Pakuti moyo wathu waweramira kufumbi, pamimba pathu pakangamira dziko lapansi.


Ukani, tithandizeni, tiomboleni mwa chifundo chanu.


Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.


Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani; titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.


Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.


Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.


Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa