Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 2:18 - Buku Lopatulika

18 Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 2:18
42 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.


Ndani uyu adetsa uphungu, ndi mau opanda nzeru?


Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kuchulukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutali; ndipo wadzichepetsa wekha kufikira kunsi kumanda.


Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu waowao, chinkana sanaone kanthu.


Koma kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziwe, adzaulemekeza ndi golide, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.


popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'chija cha Peori.


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.


Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.


Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,


pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?


Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.


Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.


Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.


Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.


Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.


Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;


Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao,


Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.


Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti tichite mau onse a chilamulo ichi.


ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.


Zimene zili naotu manenedwe a nzeru m'kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.


Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.


Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;


pofuna kukhala aphunzitsi a malamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi.


Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,


okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;


Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.


Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.


Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa