Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 3:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono ine, abale, sindidathe kulankhula nanu monga momwe ndimalankhulira ndi anthu amene ali ndi Mzimu Woyera. Koma ndidaayenera kulankhula nanu ngati anthu odalira zapansipano, kapenanso ngati ana akhanda m'moyo wanu wachikhristu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo abale sindikanakuyankhulani ngati auzimu koma adziko lapansi, makanda chabe mwa Khristu.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 3:1
11 Mawu Ofanana  

Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.


Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.


Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.


Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.


Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;


Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.


Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mau a chilungamo; pakuti ali khanda.


Ndikulemberani, tiana, popeza machimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa