Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 2:14 - Buku Lopatulika

14 Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 2:14
36 Mawu Ofanana  

Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; koma wozindikira saona vuto m'kuphunzira.


Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.


Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji?


Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye;


ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.


Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.


Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.


Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?


Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga.


Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.


Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.


Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.


koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.


koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.


Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.


Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwe Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.


koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa;


Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao.


lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.


Koma chauzimu sichili choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu.


Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.


Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu.


Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda.


Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.


Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe achibadwidwe, osakhala naye Mzimu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa