Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 1:22 - Buku Lopatulika

22 koma tsopano anakuyanjanitsani m'thupi lake mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda chilema ndi osatsutsika pamaso pake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 koma tsopano anakuyanjanitsani m'thupi lake mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda chilema ndi osatsutsika pamaso pake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho

Onani mutuwo Koperani




Akolose 1:22
21 Mawu Ofanana  

Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye, ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga.


Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake; ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pake.


Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; ndi nyenyezi siziyera pamaso pake;


Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


m'chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse.


Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso.


Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.


podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.


Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;


monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.


kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.


amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;


Pakuti Mulungu sanaitane ife titsate chidetso, koma chiyeretso.


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha.


pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake;


akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.


Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa