Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a Mulungu Okhudza Kukula Mwauzimu

110 Mau a Mulungu Okhudza Kukula Mwauzimu

Ndikufuna ndikuuzani, inu nokha, kuti munthu amene akuonetsa chikondi cha Mulungu ndi amene amadziwa zolakwa zake, kusintha khalidwe lake, kenako n’kuthandiza ena kuzungulira kwake kuti nawonso asinthe.

Kukula mwauzimu kumatanthauza kumvetsa kuti tonse ndife ochimwa, koma chifukwa cha dipo la Khristu, tingapeze chikhululukiro. Munthu wokhwima mwauzimu sadzifunsa zolakwa za ena kuti aziulula, koma adzakonza ndi chikondi ndi nzeru.

Mulungu amafuna kuti anthu ake akule mwa Iye kuti athe kuthana ndi mavuto a dziko lino popanda kutafuka mtima, podalira kuti zonse n’zotheka mwa Khristu amene amatilimbitsa.

Masiku ano, n’kofunika kwambiri kugwiritsitsa Mzimu Woyera kuti atitsogolere m’malo modziletsa ndi maganizo ndi zokhumba zathu.

Njira yokhayo yoti tilimbike motsutsana ndi machitidwe a dziko lino komanso kuti tisapatuke ku maganizo a Mulungu ndi kulola kuti Khristu apangidwe mwa ife, kufikira msinkhu wake, ndi kutsatira kaganizidwe kake ndi moyo wake.




Aefeso 4:13-15

kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14-15

Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:1-3

Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu, pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe. Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima. Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha, nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo. Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza. Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu; chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba; a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha. m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki. Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:12-14

Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mau a chilungamo; pakuti ali khanda. Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:13

kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15

koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:18

Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:14

Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:6

Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:11

Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:20

Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:17-18

kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye; ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:48

Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:1-3

Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo. Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu, ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani. Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho. Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto. Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu. Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao; Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi; ndiponso Ambuye azindikira zolingirira za anzeru, kuti zili zopanda pake. Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu; ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu; koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu. pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:1-3

Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao, Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse. Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi. Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao, odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo. ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; Koma inu simunaphunzire Khristu chotero, ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu; kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi. Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake. Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo mdierekezi. Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa. Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva. ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:22-23

kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:11

Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1

Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1-2

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro. Taonani, malembedwe aakuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu. Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu. Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:16-17

Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:6

Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14

Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:2-4

Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi. pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:15-16

Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:12-14

Ndikulemberani, tiana, popeza machimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake. Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate. Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:10

Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:2

lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:12-13

Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:23-24

Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24-25

Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:7-8

koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo; pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:13-14

Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani. Zanu zonse zichitike m'chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:17

Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo; koma wosiya chidzudzulo asochera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:16

Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:13-14

Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-19

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi, mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28

amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:29

Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:5-8

Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi. Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:33

Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:20

Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:17

M'menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m'dziko lino lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:1

Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:13-15

Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu; monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:130

Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:6-7

Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye, ozika mizu ndi omangiririka mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31-32

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani? Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:2

Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:1-3

Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11-12

Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:15

Mtima wa wozindikira umaphunzira; khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:6

Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:11

Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:8

angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22

Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:5-6

Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:3

Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:14

koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:17

Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:39

Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:14

Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3-5

Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro. Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 3:13

komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:4

Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:5

Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7-8

Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11

Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:20

Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:32

Ndidzathamangira njira ya malamulo anu, mutakulitsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:10

kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:147-148

Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu. Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:13-14

Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:9

amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:12-13

Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wokondedwa, lero ndikufuna kukutamandani ndi kukupatsani ulemerero pa zonse zomwe mumandipangira. Ndikufuna kukudalitsani ndi kuyamika chifukwa simundisiyapo chikondi chanu, chakhalapo nthawi zonse. Mwakhalako pafupi nane kundithandiza, kundilangiza, kundikumbatira, kunditonthoza ndi kundipatsa mtendere. Zikomo chifukwa cha zonse zomwe ndili nazo, mwapereka inu. Ndikupempha kuti mundithandize kukhalabe mwa inu, sindikufuna kuti mitsinje ya dziko lino indichotse cholinga chanu pa moyo wanga. Koma mundithandize kukhwima kuti ndikhale wolimba pamavuto, musalole kuti ndilephere, musalole kuti masomphenya anga asokonezeke. Ndikupemphani kuti mundithandize kukuonani nthawi zonse ndipo kuti ndikhale ngati inu. Chifukwa chake, sinthani machitidwe anga, bwezeretsani mzimu wolungama mkati mwanga ndipo pangani mwa ine mtima wofanana ndi wanu, kuti cholinga changa chachikulu chikhale kufikira msinkhu ndi muyeso wa Khristu. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa