2 Timoteyo 1:9 - Buku Lopatulika9 amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe. Onani mutuwo |
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.