Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 5:14 - Buku Lopatulika

14 Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 5:14
24 Mawu Ofanana  

chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.


Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.


Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha chimenechi, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso chuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera milandu;


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


M'khutumu simuyesa mau, monga m'kamwa mulawa chakudya chake?


Pakuti khutu liyesa mau, monga m'kamwa mulawa chakudya.


Kodi pali chosalungama palilime panga? Ngati sindizindikire zopanda pake m'kamwa mwanga?


Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga.


Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.


Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.


Iye adzadya mafuta ndi uchi, pamene adziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino.


Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.


Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai.


Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;


ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,


kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu.


Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu;


Yesani zonse; sungani chokomacho,


koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo;


Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,


Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa