Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


153 Mauthenga a Mulungu Okhudza Ziwanda

153 Mauthenga a Mulungu Okhudza Ziwanda

Ndikufuna tikambirane za Satana ndi ziwanda zake. Inde, amapezeka m’Baibulo ndipo nthawi zina amaoneka owopsa komanso amphamvu. Koma chofunika kukumbukira ndi chakuti Mawu a Mulungu amanena kuti Yesu Khristu ndi wamphamvu kuposa iwo ndipo wawagonjetsa kale.

Mulungu ndi wamphamvu kuposa mphamvu iliyonse yoipa, ndipo Yesu watipatsa ife mphamvu pa ziwanda m’dzina lake. M’buku la Aefeso 6:12a, Baibulo limatiuza kuti, “Pakuti sitilimbana ndi anthu a thupi ndi mwazi, koma ndi maulamuliro, ndi amphamvu, ndi olamulira a dziko la mdima lino, ndi mizimu yoipa ya kumwamba.”

Timadziwa kuti tikukhala m’dziko lauzimu, ngakhale maso athu sangawone nthawi zonse. Nkhondo yathu si yolimbana ndi anthu, koma ndi mizimu yoipa yomwe imawagwira ndi kuwalamulira maganizo awo. Baibulo limatiuza kuti, “Muziyimirira Satana, ndipo adzakuthawani.”

Monga thupi la Khristu, Mulungu watipatsa mphamvu ndi ulamuliro wonse wakutemberera ziwanda. Choncho usachite mantha. Dziveke chiyero ndipo utengere ziwanda m’dzina lamphamvu la Yesu.

Mdima ukamakugwira, kumbukira kuti mphamvu imapezeka m’Mawu a Mulungu. Mulungu watipatsa lonjezo la chitetezo chake ndipo watipatsa zida zofunikira kuti tizitha kulimbana ndi mayesero ndi ziwanda za mdani. Ngakhale ziwanda zili zenizeni, sitiyenera kuziopa. M’malo mwake, tiyenera kugwira zolimba malonjezo ndi mphamvu ya Mulungu.




Mateyu 8:16

Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:1

Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:1

Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:17-20

Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba. Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse. Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake. Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:17

Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai; milungu yosadziwa iwo, yatsopano yofuma pafupi, imene makolo anu sanaiope.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:15

atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:20

Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:11

Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:2

Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:31

Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:22

Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:14

pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:15-16

Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani? Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawagonjetsa onsewo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:34

Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:25

Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:9

Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:24-26

Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako; ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka. Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:14

Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:28-34

Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu panjira imeneyo. Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike? Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka. Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya. Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo. Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi. Koma akuziweta anathawa, namuka kumzinda, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja. Ndipo onani, mzinda wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m'malire ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:18

Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:1-20

Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa. Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko. Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri. Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mzinda, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho. Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo. Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m'malire ao. Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo. Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:27-39

Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumzinda, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda. Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau aakulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze. Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu. ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao. Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye. Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya. Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola. Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nkulowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa. Ndipo akuwetawo m'mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza okhala mumzinda ndi kuminda. Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa. Ndipo amene anaona anawauza iwo machiritsidwe ake a wogwidwa chiwandayo. Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera. Ndipo munthuyo amene ziwanda zinatuluka mwa iye anampempha Iye akhale ndi Iye; koma anamuuza apite, nanena, Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumzinda wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:22

Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:34

Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:23-26

Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye. Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu. Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye. Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau aakulu, unatuluka mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:33-36

Ndipo m'sunagoge munali munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti, Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu. Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse. Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:24

Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:22

Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10-11

Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:18

Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:14-18

Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati, Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi. Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa. Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno. Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:39

Ndipo analowa m'masunagoge mwao mu Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:16-18

Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake. Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso. Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:44

Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:24

Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:17

Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:32-34

Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda. Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele. Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:41

Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiye Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:14-15

Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chao chidzakhala monga ntchito zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:43-45

Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza. Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa. Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:27

ndiponso musampatse malo mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:9

Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:22-28

Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda. Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu. Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israele. Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine. Ndipo Iye anayankha, nati, Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagalu. Koma iye anati, Eetu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao. Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:1

Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 2:11

kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:20-21

Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda. Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:25-30

Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake. Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake. Ndipo ananena naye, Baleka, ayambe akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu. Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Inde Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana. Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi. Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu; Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 17:7

Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:37

Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:8

Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:13

Ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:16

Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 16:14

Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 21:6

Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 8:19

Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 10:13

Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:24-28

Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda. Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mzinda uliwonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala; ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake? Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu. Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:6

Angelonso amene sanasunge chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:4

Pakuti ngati Mulungu sanalekerere angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:2

zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:20

Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:7

Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawatulukira, yofuula ndi mau aakulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:3

Ndipo Satana analowa mwa Yudasi wonenedwa Iskariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:20-21

Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda; ndipo sanalape mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:18

ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 13:32

Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:41

Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 26:18

kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:39

ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:8

Pakuti ananena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:42

Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:18

Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:19

Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:31-32

Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu; koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:18

chifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana anatiletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:5

kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 2:1-7

Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova. Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake. Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa. Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao. Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukulu ndithu. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa. Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wake wokha uuleke. Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:23

Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:38

za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:10

Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:8

iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:19

Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:24

chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:3

Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:11

ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:15

pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:18

Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:15

Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:38-39

Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa sanalikutsata ife. Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:10

Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:18

Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:4

mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:29

Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:2

Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:27

Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:25

koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:21

pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:79

Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:14

Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:31

Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:11-12

Ndipo Mulungu anachita zamphamvu za pazokha ndi manja a Paulo; kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:15

ndi kuti akhale nao ulamuliro wakutulutsa ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:15

Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:31

Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:13

Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:1-2

Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu pakuti kwalembedwa kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize. Ndipo, Pa manja ao adzakunyamula iwe, kuti ungagunde konse phazi lako pamwala. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako. Ndipo mdierekezi, m'mene adamaliza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi ina. Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira. Ndipo Iye anaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalemekezedwa ndi anthu onse. Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata. Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa, Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika, kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye. kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:13

Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:13

Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:15

Sindipempha kuti muwachotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:15

Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:26

ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:3

Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:15

Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:30

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:37

Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:1-3

Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda, Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira. Lamulira izi, nuziphunzitse. Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima. Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza. Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu. Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe. m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m'chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto; a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:3

ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 6:7

Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:32

amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:31

Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:2

ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:7-9

Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikaele ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinapambane, ndipo sanapezekenso malo ao m'mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:18-23

Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama, nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti aliyense amene ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera. Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu. Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako. Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:9

Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 3:1

Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 4:18

Taona, sakhulupirira atumiki ake; nawanenera amithenga ake zopusa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:30

Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:28

Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:11

za chiweruzo, chifukwa mkulu wa dziko ili lapansi waweruzidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:21-22

Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere; koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:19

Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:11

Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 3:1-2

Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye. Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 18:21

Nuti uwu, Ndidzatuluka ndi kukhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; tuluka, ukatero kumene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:53

Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 6:4

Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 16:23

Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:10-12

Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:1-4

Ndipo mngelo wachisanu anaomba lipenga, ndipo ndinaona nyenyezi yochokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye chifunguliro cha chiphompho chakuya. Ndipo lili nayo michira yofanana ndi ya chinkhanira ndi mbola; ndipo m'michira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu. Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni. Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso matsoka awiri m'tsogolomo. Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga, ndipo ndinamva mau ochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolide lili pamaso pa Mulungu, nanena kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pamtsinje waukulu Yufurate. Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu. Ndipo chiwerengero cha nkhondo za apakavalo ndicho zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi; ndinamva chiwerengero chao. Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulufure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao mutuluka moto ndi utsi ndi sulufure. Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulufure, zotuluka m'kamwa mwao. Pakuti mphamvu ya akavalo ili m'kamwa mwao, ndi m'michira yao; pakuti michira yao ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo aipsa nayoyo. Ndipo anatsegula pa chiphompho chakuya; ndipo unakwera utsi wotuluka m'chiphomphomo, ngati utsi wa ng'anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, chifukwa cha utsiwo wa kuchiphomphocho. Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda; ndipo sanalape mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao. Ndipo mu utsimo mudatuluka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko zili ndi mphamvu. Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena chabiriwiri chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pao ndiwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:30

Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:36

Ndipo anati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:38-39

Ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo; ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Wamkulu ndi woopsa Yehova, woyenera kutamandidwa ndi kukwezedwa, dzina lake liposa dzina lililonse, Iye ndi wamuyaya ndi waulemerero, Woyera ndi woopsa. Pamaso pake mafumu amagwada, mizimu yoipa imathawa, palibe mphamvu ya mdima yomwe ingamutsutse. Iye ndiye Ine Ndine, wamphamvu ndi wosagonjetseka. Ndimakulambirani chifukwa chakuti ndinu ndani, ndimakulambirani chifukwa cha momwe munalili ndi zonse zomwe munachita. Zikomo chifukwa ndatetezedwa ndi mwazi wanu, ndipo pamaso panu palibe chomwe chingandikhudze. Munagonjetsa mdani wanga ndipo munandipatsa chigonjetso pa iwo pa mtanda wa pa Gologota. Zikomo chifukwa sindingaope choipa chilichonse, ndodo yanu ndi chibonga chanu zimandilimbikitsa. Ngakhale mdani ataukira ngati mtsinje, inu mumakweza mbendera ya chigonjetso. Chifukwa chake sindingaope gulu lankhondo lomwe lingandilimbane nalo, chifukwa mtima wanga uli mwa inu. Zikomo Ambuye, chifukwa ndinu chitetezo changa ndipo mumaletsa mizimu yoipa yonse yomwe ikufuna kundiwukira ndi mphamvu ya dzina lanu. Ndimakulambirani ndi kukukwezani kosatha. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa