Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:2 - Buku Lopatulika

2 ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Panalinso azimai ena amene Yesu adaaŵatulutsa mizimu yoipa ndi kuŵachiza nthenda zina. Azimaiwo ndi aŵa: Maria, wotchedwa Magadalena, (amene mwa iye mudaatuluka mizimu yoipa isanu ndi iŵiri);

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 komanso akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi matenda: Mariya, wotchedwa Magadalena, amene mwa iye munatuluka ziwanda zisanu ndi ziwiri;

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:2
11 Mawu Ofanana  

Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.


Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.


Ndipo unamtsata unyinji waukulu wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pachifuwa, namlirira Iye.


Ndipo omdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, anaima kutali, naona zinthu izi.


Ndipo akazi, amene anachokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wake.


Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.


Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala.


Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa