Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 12:24 - Buku Lopatulika

24 Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Koma Afarisi atamva zimenezi adati, “Iyai, mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa sizichokeratu kwina, koma kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Koma Afarisi atamva zimenezi, anati, “Uyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mkulu wa ziwandazo.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:24
7 Mawu Ofanana  

Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.


Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?


Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda.


Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.


Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.


Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.


Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa