Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:42 - Buku Lopatulika

42 Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Pamene mwanayo ankabwera, mzimu woipawo udamgwetsa pansi nkumuzunguza kolimba. Koma Yesu adazazira mzimu woipawo. Kenaka atamchiritsa mwanayo, adamperekanso kwa bambo wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake.

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:42
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku chipinda chosanja, nalowa naye m'nyumba, nampereka kwa amake; nati, Eliya, Taona, mwana wako ali moyo.


Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunamu uja. Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako.


Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu.


Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.


ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.


Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.


Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,


Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha.


Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.


Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa