Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Yesu adati, “Ha! Anthu a mbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo. Ndiyenera kukhala nanube ndi kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwana wanuyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Yesu anayankha kuti, “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:41
31 Mawu Ofanana  

Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israele.


Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikike ndi Mulungu.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?


Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.


Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.


Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri;


Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.


Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo.


Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.


Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono.


Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?


Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.


Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.


Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo m'kuchita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?


Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe.


Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.


Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikire, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?


Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.


Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'chipululu.


Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.


Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?


Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema nchao; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.


Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanathe kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.


Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.


Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.


kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa