Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 10:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 10:1
26 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo pakufika madzulo, Iye analinkukhala pachakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri;


Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.


Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.


Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.


Ndipo kutacha, anaitana ophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawatchanso dzina lao atumwi:


monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.


Yohane anayankha nati, Munthu sangathe kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba.


Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lake.


Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?


Ndipo chizindikiro chachikulu chinaoneka m'mwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa