Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:25 - Buku Lopatulika

25 koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Koma anthu onse ali m'tulo, mdani wake adabwera, nkufesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:25
19 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndili m'tulo, namuika m'mfukato mwake, naika mwana wake wakufa m'mfukato mwanga.


Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;


Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.


Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo?


Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.


Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.


ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.


Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.


ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.


ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.


Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.


Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa