Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:53 - Buku Lopatulika

53 Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

53 Masiku onse, pamene ndinali ndi inu m'Kachisi, simunatansa manja anu kundigwira: koma nyengo yino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

53 Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu, inuyo osandigwira. Koma ino ndi nthaŵi yanu ndiponso ya mphamvu za mdima.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

53 Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:53
20 Mawu Ofanana  

kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba?


Ndipo pamenepo anamgwira Iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutali.


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anatuluka pomwepo. Koma kunali usiku.


Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;


Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.


Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe aakulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenge Iye bwanji?


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.


amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa