Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:52 - Buku Lopatulika

52 Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Kenaka Yesu adalankhula nawo onse amene adaabwera kudzamugwira, akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso akulu a Ayuda. Adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga ngati kuti ndine chigaŵenga?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga?

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:52
10 Mawu Ofanana  

Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova.


Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.


Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.


Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro.


Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo.


Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lake, namchiritsa.


Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa